Here’s today’s lineup on Channel Africa, based on the official schedule:




Your favourite in one place — stay updated and in the running.
Enter exciting contests and giveaways. Stay tuned for chances to win exclusive Channel Africa merchandise and experiences.
Explore African rhythms, curated playlists, and artist spotlights from across the continent. Celebrate the sound of Africa with curated playlists.
Catch your favourite programs live or on-demand. From current affairs to cultural deep-dives, there’s something for every listener.
Listen to thought-provoking conversations, investigative series, and stories that matter — anytime, anywhere.
Your favourite in one place — stay updated and in the running.






























































































































The voices behind Channel Africa — passionate storytellers, journalists, and broadcasters from across the continent.
It's time for #YourVoiceAfrica
Today's question:
Opposition groups in Zimbabwe have announced their withdrawal from the ongoing public consultations on the Constitution Amendment Bill No. 3, citing violent scenes during hearings in Harare.
What do you want to ...see happen in Zimbabwe regarding the recent actions that has been taking place at the public hearings?
Share your thoughts with @MphoKSithole in the comments or send a voice note on WhatsApp: ️+27 83 288 6684
Your voice matters. Let Africa hear you.
#AfricaWorldHour #ChannelAfrica
#AfricaWorldHour welcomes @mphoksithole!
Join her weeknights from 21:00 – 22:00 CAT for trusted updates on continental and global news, bringing Africa closer to the stories shaping the world 🌍 🗞️
Be part of the conversation.
#AfricaWorldHour #ChannelAfrica
#AfricaWorldHour welcomes @mphoksithole!
Join her weeknights from 21:00 – 22:00 CAT for trusted updates on continental and global news, bringing Africa closer to the stories shaping the world 🌍 🗞️
Be part of the conversation.
#AfricaWorldHour #ChannelAfrica
#Zochitika
Nkhani za masewera
>Timu ya mpira wamiyendo yadziko la Democratic Republic of Congo (DRC), yakwanitsa kulowa mu mpikisano wa World Cup koyamba m'zaka zokwana makumi asanu ndi ziwiri. Chigoli cha Axel Tuanzebe mu nthawi yowonjezera chagonjetsa anyamata a Reggae, timu ...yadziko la Jamaica 1-0 mu masewera ama play-off pabwalo la Guadalajala mdziko la Mexico. Tuanzebe, amene amasewera ndi Burnley yamdziko la England, anagoletsa chigoli chokhacho cha masewerawo kutumiza timuyo ku World Cup kumene akakumane ndi Portugal, Colombia, ndi Uzbekistan m'gulu K. Izi, zikutanthauza kuti dziko la pakati pa Africa likasewera koyamba mu mpikisanowu kuyambira chaka cha 1974 mdziko la German pamene timuyi inkadziwika kuti Zaire, ndipo inagonjetsedwa ndi Scotland, Yugoslavia, ndi Brazil.
>Timu ya Kaizer Chiefs yamdziko la South Africa yachita chikondwerero cha mbiri yake dzulo lachiwiri pa 31 mwezi wa Marichi, pokhazikitsa timu yawo ya azimayi ya Kaizer Chiefs Women's Team. Kukhazikitsaku kwayimira gawo lofunika kwambiri kwa mpira wa azimayi mdziko la South Africa. Chiefs yalowa m'nyengo yatsopano, yachitukuko, kupatsa mwayi azimayi kuwala pa mlingo wapamwamba. Amene analengeza zankhaniyi pa msanja ya mwambo okhazikitsa timuyi, anali Jessica Motaung, wamkulu wotsogolera kutsatsa timuyi, ndipo anati ndi chinthu chimene wakhala akulota kwa zaka zambiri.......
>Kalusha Bwalya, katswiri wakale wamasewera a mpira wamdziko la Zambia, wachenjeza kuti mpikisano wa FIFA World Cup sukakhala ophweka kwa matimu a mu Africa, koma akukhulupilira kuti Africa ili ndi chiyembekezo chatsopano mpikisanowu utakulitsidwa. Pamene matimu a mu Africa omwe atenge nawo mbali mu mpikisanowu awonjezeredwa pafupifupi kawiri, Africa ili ndi mwayi wawukulu okapanga zodabwitsa, komanso kukapanga bwino. Kalusha Bwalya, amene anapata mphotho ya wosewera bwino kwambiri mu Africa, kapena kuti African Footballer of the Year mchaka cha 1988, wawuza gawo lowulutsa za masewera la SABC momwe kukulitsidwa kwa mpikisanowu kungasinthire mwayi wa matimu a mu Africa......
>Timu yadziko la Iran itenga nawo mbali mu mpikisano wa FIFA World Cup, ndipo masewera awo adzachitikira mdziko la United States of America monga momwe zinakonzedwera. Umu, ndi malingana ndi Gianni Infantino mtsogoleri wa FIFA. Pakhala pali kusatsimikizika timu ya Iran kutenga mbali mu mpikisanowu chifukwa cha nkhondo yomwe ilipo pakati padziko la US, mogwirizana ndi dziko la Israel, kulimbana ndi dziko la Iran. Koyambirira kwa mwezi uno bungwe loona za mpira wamiyendo mdziko la Iran linanena kuti likukambirana ndi FIFA kuti masewera awo asamutsidwe kuchokera ku US kupita ku Mexico. Iran ikuyembekezeka kukumana ndi New Zealand ndi Belgium mu mzinda wa Los Angeles pa 15 ndi pa 21 mwezi wa Juni, komanso Egypt mu mzinda wa Seattle pa 26 mwezi womwewo wa Juni. Mpikisanowu, umene uyambe pa 11 mwezi wa Juni, uzachitikira m'mayiko atatu, US, Canada, ndi Mexico. Mtsogoleri wadziko la Mexico, Claudia Sheinbaum, ananena kuti dziko lake ndi lokonzeka kulandira masewera a Iran, koma Infantino wati ayi, zichitika monga zakonzedwera.
Alex Nkhuku
Channel Africa News.
#ZOCHITIKA
MU NKHANI ZATHU ZA CHUMA
#Dziko la Britain, likuyembekezeka kukhazikitsa msonkhano pomwe nthumwi zochokera mmaiko makumi atatu zikuyembekezeka kutenga nawo gawo pa kufuna kukambirana nkhani zokhudza mafuta omwe akadali otsekerezedwa pa njira ya pa nyanja ya Strait of ...Hormuz. Nduna yaikulu ya dziko la Britain Keir Starmer, ndi yomwe yalengeza za msonkhanowu.
#Bungwe lotolela msonkho mdziko la South Africa, la South African Revenue Services, SARS, lati latolera msonkho wa ndalama zokwana $117 billion. Ndipo aka ndi koyamba bungweli kutolera msonkho otere chikhazitsikidwileni cha bungweli. Komishonala wa bungweli, Edward Kiewswetter, yemwe teremu yake ya zaka zisanu ndi ziwiri iifike kumapeto kwa mwezi wa mawa, ndi yemwe walengeza izi pa msonkhano wa atolankhani masana ano.
#Bungwe loona za malonda a mbewu ya tea mdziko la Kenya, la Tea Traders Association, lati kusokonekera kwa mayendedwe a katundu chifukwa cha mikangano yomwe ikuchitika ku maiko a aluya, kwapangitsa kuti malonda a tea olemera ndi 8 million atsekerezedwe pa doko la Mombasa. Bungweli, lati chiyambireni pa 1 Marichi, tea yemwe wakhala akutsekerezedwa pa dokoli, akupangitsa bungweli ndi alimi ake kutaya ndalama yokwana $8 million pa sabata.
Thamo Kapisa
Channel Africa News
#ZOCHITIKA
NKHANI ZATHU ZA LERO PA CHINYANJA
#Presidenti wa dziko la USA Donald Trump, wati akuganiza zotulutsa dziko la USA mu bungwe la North Atlantic Treaty Organization, NATO. Trump, waonjezera kunena kuti akuganiza motere chifukwa akuona kuti bungweli si lodalirika.
...Trump, walankhula izi patangodutsa ma ora angapo kulankhula kunena kuti ali okonzeka kuchotsa asilikali a dzikolo ku dziko la Iran mmasabata awiri akubwerawa.
Mtolankhani wa BBC Paul Adams, wafotokoza kunena kuti zikuonena ngati Trump ali okhumudza ndi maiko a mu bungweli omwe akana kumuthandiza kulowelerapo pa mikangano yomwe ikuchitika pakati pa dzikolo ndi dziko la Iran.
#Mtsogoleri wa dziko la Senegal, Bassirou Diomaye Faye, wasaina lamulo latsopano lokhudza kupereka chilango chokhala kundende kwa zaka khumi kwa anthu ochita mchitidwe wa umathanyula(same-sex relations), pachingelezi.
Lamuloli, likuletsanso kulimbikitsa kapena kufalitsa nkhani zokhudza maukwati a akazi kapena amuna okhaokha, zomwe zadzetsa maganizo osiyanasiyana kwa anthu komanso mabungwe omenyera ufulu wa anthuwa padziko lonse.
Lamuloli, linavomerezedwa ndi nyumba ya malamulo ya m'dzikolo kumayambilo kwa mwezi watha, ndipo kuvomelezedwa kwa lamuloli ndi mtsogoleriyu kukutanthauza kuti tsopano onse omwe azilimbikitsa mchitidwe ogonana komanso kukwatilana akazi kapena amuna okhaokha nawonso adzimangidwa.
Bassirou Diomaye Faye, komanso nduna yaikulu ya dzikolo a Ousmane Sonko, analonjeza anthu a m'dziko la Senegal nthawi yomwe amachita misonkhano yokopa anthu kuti adzabweletsa malamulo okhwima pankhani yokhudza maukwati a amuna kapena akazi okhaokha ndipo kukhazikitsidwa kwa lamuloli kwakwaniritsa lonjezo lawo.
#Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) lati kusintha kwa mitengo ya mafuta a galimoto komanso mafuta a ndege kwachitika kaamba ka nkhondo ya pakati pa maiko a USA, Israel komanso Iran.
Nkhondo ya pakati pa maiko atatuwa idayamba masabata anayi apitawa zomwe zatsokoneza ntchito za malonda kuphatikiza kayendedwe ka mafuta pa nyanja makamaka maiko aku Middle East.
Mkulu wa bungweli Dad Chinthambi wati nkhondoyi yachititsa kuti mafuta pa misika yakunja akwere zomwe zakhudzanso mitengo ya mafuta a galimoto pa misika ya mdzikolo.
A Chinthambi ati bungweli layesetsa kuunikira kuti anthu mdziko muno asakhudzidwe kwambiri ndi kusinthaku, ndipo kuti kampani zoitanitsa mafutawa zipitilire kuitanitsa mafutawa.
Padakali pano, bungweli lakweza mitengo ya mafuta a Petulo ndi 34% kuchoka pa k4,965 nkufika pa K6 672 pa lita, ndipo dizilo wasintha ndi 35% kuchoka pa K4,945 nkufika pa K6, 687. Ndipo mafuta andege akweranso pafupifupi ndi 80%.
#Bungwe loona za kayendetsedwe ka masankho mdziko la South Africa la Independent Electoral Commission of South Africa, lati atsogoleri oposa 100 000 ndi omwe akuyembekezeka kudzapikisana nawo pa masankho osankha ma khansala pa masankho a a maboma aang'ono ang'ono omwe akuyembekezeka kuchitika mdzikoli kumapeto kwa chaka chino. Mipando ya makhansala okwana pafupifupi 9 600 ndi yomwe ikuyemekezeka kukhazikitsa adindo atsopano ochokera mzipani zosiyana siyana. Mkulu wa bungwe la IEC, Sy Mamabolo, wati chiwerengerochi ndi kukwera kusiyana ndi pa masankho a maboma aang'ono ang'ono omwe anachitika mu chaka cha 2021. Mamabolo, walankhula motere pa mwambo okhazikitsa ndondomeko zina za mu bungweli monga chizindikiro kapena kuti logo, chatsopano cha bungweli.
Thamo Kapisa
Channel Africa News
[Tili lomodzi pa mphepo] 🌍✨
Chaka chatsopano, chiyambi chatsopano.
#Zochitika yabwera ndi pulogalamu yake yoyamba ya chaka chino malingana ndi kalendala ya wayilesi ino ya Channel Africa , Zochitika izikubweretserani nkhani zosangalatsa, zokamba zofunika, komanso malingaliro ...ochokera m’madera osiyanasiyana a mu Africa.
Tikhale limodzi kuyambira 19:00 – 20:00 CAT pamene tikupitiriza kukudziwitsani, kukulimbikitsani kulumikizana, ndi kugwirizanitsa Africa.
#Zochitika #ChannelAfrica
Subscribe to our newsletter and stay informed with the latest news, program highlights, and exclusive content from Channel Africa — a trusted voice in global broadcasting.
Channel Africa promotes Africa’s national interests through innovative content aiding the continent’s development. We deliver news, current affairs, and cultural programming globally, broadcasting in multiple languages to connect Africa to the world and the world to Africa.