Welcome to Channel AFRICA

The African
Beat, Beauty
& Strength

Today's Line Up

Here’s today’s lineup on Channel Africa, based on the official schedule:

Morning Reset
03:00 - 06:00

Morning Reset

Previous
GO TO SHOW
Rise and Shine
06:00 - 09:00

Rise and Shine

Previous
GO TO SHOW
On The Move
09:00 - 12:00

On The Move

Previous
GO TO SHOW
Africa Update
12:00 - 13:00

Africa Update

Previous
GO TO SHOW

Your Favorites

Your favourite in one place — stay updated and in the running.

Advert Banner Alt

Enter exciting contests and giveaways. Stay tuned for chances to win exclusive Channel Africa merchandise and experiences.

Advert Banner Alt

Explore African rhythms, curated playlists, and artist spotlights from across the continent. Celebrate the sound of Africa with curated playlists.

Advert Banner Alt

Catch your favourite programs live or on-demand. From current affairs to cultural deep-dives, there’s something for every listener.

Advert Banner Alt

Listen to thought-provoking conversations, investigative series, and stories that matter — anytime, anywhere.

Live Activity Update.

0

Competitions

2

Events

1

Polls

Featured Content

Your favourite in one place — stay updated and in the running.

More Presenters

The voices behind Channel Africa — passionate storytellers, journalists, and broadcasters from across the continent.

[On-Air]
Deputy Minister of South Africa’s Cooperative Governance and Traditional Affairs (@NationalCoGTA), Prince Zolile Burns-Ncamashe, has urged calm in KuGompo, Eastern Cape, following a protest against the alleged coronation of an Igbo Nigerian king that turned violent.

Nwobi ...Smart, Human Rights Attorney and President General of the Nigerian Union South Africa (NUSA), weighs in in conversation with @TsepisoMakwetla.

#AfricaWorldHour #ChannelAfrica #SouthAfrica #EasternCape #NUSA #Nigeria #IgboKingSouthAfrica

Wrap up your evening on an informed note with #AfricaWorldHour.

@TsepisoMakwetla brings you in-depth analysis, sharp insights, and the day’s most important stories from Africa and around the world. Thoughtful conversations to help you make sense of the headlines before the day ends.
...
#ChannelAfrica

#AfricaWorldHour, hosted by Tsepiso Makwetla is a late-night Pan-African talk show that promotes a progressive African story.

The show provides the latest updates on major news stories between 21:00 – 22:00 CAT.

#ChannelAfrica

#ZOCHITIKA

MU NKHANI ZATHU ZA CHUMA

#Maiko a Egypt ndi Cyprus asaina mgwirizano ogwilira ntchito limodzi mu gawo la za mphweya wa gasi. Maikowa, asaina mgwirizanowu pa mbali pa msonkhano otchedwa Egypt 2026 Energy Show. Mu mgwirizanowu, maikowa agwirizana kuti dziko la Egypt ...lidzigula mphweya wa gasi kuchokera ku dziko la Cyprus pansi pa makampani omwe ali mmadera a Kronos ndi Aphrodite.

#Kampani ya Microsoft, yalengeza za kukhazikitsa ndondomeko zina pa kagwiritsiridwe ntchito pa App ya Copilot, ndipo tsapano ogwiritsira ntchito adzikwanitsa kugwiritsira ntchito AI. Mwa ndondomeko ina yomwe yakhazikitsidwa, ndi yotchedwa Critique.

#Pamene mafuta a galimoto akuyembekezeka kukwera mdzikomla South Africa lachitatu sabata lino, nzika zina zayamba kuika ganizo pa kuyendela sitima pa kukafika ku malo ogwira ntchito zawo. Kampani yoona za mayendedwe a pa njanji mdzikoli, ya Passenger Rail Agency of South Africa, yatsindika kuti mitengo yokwelera ma sitima siikwera, ndipo yalimbikitsa nzika kuti ziyambe kukwera ma sitima. Mmodzi mwa akulu akulu mu kampaniyi, Raymond Maseko, wati kampaniyi imagulitsa ma tikiti a pa sabata komanso a pa mwezi onse, omwe atha kuthandiza nzika.


Thamo Kapisa
Channel Africa News

#ZOCHITIKA

NKHANI ZATHU ZA LERO PA CHINYANYA SERVICE

#Wamkulu wapampando wa bungwe loyanjanitsa maiko a mu Africa la African Union, Mahmoud Ali Youssouf, wati bungweli lili lodzipereka pa kugwira ntchito limodzi ndi bungwe la United Nations pa kufuna kupeza njira zothana ndi ...mikangano yomwe ikuchitika mdziko la Sudan.
Youssouf, walankhula izi pa mkumano ndi nthumwi yoimilira mlembi wamkulu wa bungwe la UN mdziko la Sudan, Pekka Haavisto.

#Adindo mdziko la Nigeria, akhazikitsa zikhwimitso za mayendedwe mmadera ena mu mzinda wa Jos mchigawo cha Plateau State, potsatira zigawenga kuukira malo omwera mow. Pa chiwembuchi, anthu okwana khumi ndi awiri aphedwa. Polengeza za kukhazikitsa zikhwimitsozi, nduna yaikulu ya chigawochi, Caleb Manasseh Muttwang, wati kafukufuku wakhazikitsidwa pa kufuna kudziwa gulu la zigawenga lomwe lachita chiwembuchi.

#Anthu atatu omwe ndi amayi awiri ndi bambo m'modzi, amwalira pamene nyumba yosanjikizana yomwe amapempheramo inawagwera mu mzinda wa Accra mu likulu la dziko la Ghana. Ngoziyi, yachitika dzulo, ndipo malingana ndi anthu amene anaona ngoziyi ikuchitika, ati anamva kufuula kuchokera m'nyumbayi pamene anthuwa anatsekerezedwa.
Anthu opulumutsa anzawo pa ngozi, adagwira ntchito usiku onse pa kufuna kuonetsetsa kuti onse amene adatsekerezedwa apulumutsidwa ndipo pali chitsimikizo kuti palibe yemwe watsala atatsekerezedwa pa malopa.
Pa nyumbayi, panali anthu okwana makumi awiri ndi atatu ndipo nyumbayi idali mbali imodzi ya sukulu imene idamangidwa ku dera la Accra New Town koma idali itakhala zaka zambiri isadamalizidwe kumangidwa.

#Pamene patsala miyezi ingapo kuti masankho osankha mtsogoleri komanso aphungu ndi ma meyala mdziko la Zambia, ma meyala asanu pamodzi ndi makhansala makumi awiri, atuluka mzipanu zawo ndi kulowa mchipani cholamulira cha UNPD. Mtolankhani wa Channel Africa Daniel Elisha Banda, walankhula ndi Lyson Nyirenda, yemwe ndi mkulu wa nthambi ya achinyamata mchipani cha UPND mchigawo cha Estern Province, yemwe wapereka zifukwa zomwe anthuwa alowa mchipanichi.

#Komiti ya kunyumba yamalamulo mdziko la Malawi ya Public Accounts yati ipereka kunyumba yamalamulo, lipoti lake la kafukufuku okhudza ndondomeko yogula hotela ya Amaryllis posadikira umboni wa amene adali mlembi wa muofesi yamtsogoleri wa dziko a Colleen Zamba.
Wapampando wa komitiyi a Steven Malondera wanena izi mmawa uno pomwe a Zamba alephera kufika kuti aonekere ku komitiyi, kunyumba ya malamulo.
A Malondera ati woimira pa mlandu a Zamba, a George Jivason Kadzipatike, awadziwitsa kuti a Zamba ali kunja kwa dzikolo kumene akulandira thandizo la mankhwala kotero sakwanitsa kukumana ndi komitiyi lero.
Iwo ati, potengera kuti zokambirana za kunyumba ya malamulo azimaliza pa 10 Epulo, achiona chofunika kuti asadikire a Zamba ndikukapereka lipoti lawo kunyumbayi sabata ino.

#Dziko la Iran, laphulitsa mabomba angapo ku dziko la Israel , pa nthawi yomwe presidenti wa dziko la USA Donald Trump wati zokambirana zikuchitika pakati pa maiko a USA ndi Ira zofuna kuthetsa mikangano.
Pamene asilikali amdziko la Israel, alengeza kuti nawo apitiliza kuphulitsa mabomba ku dziko la Iran, maka ku mzinda wa Tehran mu likulu la dzikolo. Mtolankhani wa BBC James Waterhouse, akufotokoza kunena kuti ngakhale dziko la Israel likupitiliza kuphulitsa mabomba ku dziko la Israel, dziko la Iran lili ndi kuthekera kopitiliza kuphulitsa mabomba ku maiko a aluya komwe sabata yatha anaphulitsa bomba pa malo opnagira mafuta mdziko la Kuwait.

Thamo Kapisa
Channel Africa News

Imvani nkhani zabwino zapamwamba mwatsatane tsatane madzulo ano ndi Thamo Kapisa.

#Zochitika #ChannelAfrica #Chinyanja

[ICMI] Ayam Shekifu na timu nzima ya Kiswahili wanakuletea taarifa za kila siku kwenye Darubini Ya Afrika pekee kwenye Channel Africa📜
Sikiliza DarubiniYa Afrika kwa mengi zaidi;
▶️: youtube.com/@channelafrica1
👍: Channel Africa
🌐: bit.ly/SoundaAfrica
📱: ...@SABCPlus App

#DarubiniyaAfrika #habarizaafrika #Kiswahili

#Zochitika
Nkhani za masewera

>Lovemore Fazili, mphunzitsi wa timu yampira wamiyendo ya azimayi yadziko la Malawi yomwe imadziwikanso kuti ma Scorchers, watchula osewera ake okwana makumi atatu ndi asanu omwe akalowe ku msasa wokonzekera mpikisano wa Four Nations FIFA Series omwe ...ndi wamatimu anayi. Mpikisanowu, uchitikira mdziko la Kenya kuchokera pa 11 mpaka pa 15 mwezi wa Epulo, pa bwalo la Nyayo National Stadium. Matimu amene atenge mbali mu mpikisanowu ndi Kenya yomwe imatchukanso kuti ma Harambee Starlets, Australia, India, ndi Malawi. Malawi idzakumana ndi Australia m’masewera awo oyamba

>Bungwe loona za mpira wamiyendo mu Africa la Confederation of African Football (CAF), likhazikitsa kusintha ndi kukonza malamulo ndi ndondomeko zake, pofuna kupewa zomwe zinachitika mu ndime yomaliza ya mpikisano wa Africa Cup of Nationas (AFCON) 2025 kuti zisazachitikenso. Mtsogoleri wabungweli, Dr Patrice Motsepe, wanena kuti kusinthaku ndikufuna kubwezeretsa ndi kulimbikitsa chikhulupiliro ndi chidaliro kwa ma referee a bungwelo, makina othandizira ma referee, komanso mabungwe oweluza milandu. Motsepe walankhula kwa atolankhani pakutha kwa msonkhano wa komiti yayikulu ya CAF omwe unachitikira mu mzinda wa Cairo mdziko la Egypt lamlungu.......

>Mlembi wamkulu wa bungwe la CAF watula pansi udindo wake pa nthawi ya chipwirikiti mu mpira wa miyendo mu Africa. M'mawu ake, Veron Mosengo-Omba wati akutula pansi udindo wake, koma kuchoka kwake kwabwera chifukwa chamikangano yokhudza chigamulo cholanda timu yadziko la Senegal chikho cha mpikisano wa 2025 AFCON, komanso kuchedwetsa mpikisano wa azimayi wa Women's Africa Cup of Nations (WAFCON) mu mphindi zomaliza. Mosengo-Omba, omwe ali zaka 63, yemwenso amachokera mdziko la Democratic Republic of Congo, koma alinso nzika yadziko la Switzerland, anasankhidwa ngati mlembi wamkulu wabungwe la CAF mwezi wa Marichi chaka cha 2021. Wamkulu oyang'anira za mipikisano m'bungwe la CAF, Samson Adamu wamdziko la Nigeria atenga udindo ngati mlembi wamkulu.......

>Mtsogoleri wa bungwe la CAF, Dr Patrice Motsepe, walengeza kuti mpikisano wa Africa Cup of Nations (AFCON), ukula kuchoka pa matimu makumi awiri ndi anayi kufika pa matimu makumi awiri, asanu ndi atatu. Kusinthaku, kumene kwabwera mwadzidzidzi pambuyo pa msonkhano wa komiti yayikulu ya bungweli, cholinga chake ndi kuwonetsa luso la osewera ambiri ochokera m'mayiko osiyanasiyana a mu Africa, ngakhale tsatanetsatane wa momwe mpikisanowu usunthidwe, ndi nthawi yake, sizinanenedwe bwinobwino. Motsepe watsimikiza kuti mpikisano wa AFCON wa chaka cha 2027 uchitika momwe anakonzera m'mayiko a Kenya, Tanzania, ndi Uganda. Kuphatikizira apo, padzakhalanso mpikisano wina wa AFCON mchaka cha 2028, kenako usintha kumachitika pa zaka zinayi zilizonse. Bungwe la CAF likukonzanso kuyambitsa mpikisano watsopano wa Nations League kuyambira chaka cha 2029 pomwe matimu khumi, asanu ndi imodzi azikumana pa zaka ziwiri zilizonse.

Alex Nkhuku
Channel Africa News.