Here’s today’s lineup on Channel Africa, based on the official schedule:




Your favourite in one place — stay updated and in the running.
Enter exciting contests and giveaways. Stay tuned for chances to win exclusive Channel Africa merchandise and experiences.
Explore African rhythms, curated playlists, and artist spotlights from across the continent. Celebrate the sound of Africa with curated playlists.
Catch your favourite programs live or on-demand. From current affairs to cultural deep-dives, there’s something for every listener.
Listen to thought-provoking conversations, investigative series, and stories that matter — anytime, anywhere.
Your favourite in one place — stay updated and in the running.





























































































































The voices behind Channel Africa — passionate storytellers, journalists, and broadcasters from across the continent.
#ZOCHITIKA
MU NKHANI ZATHU ZA CHUMA
#Akatswiri pa nkhani za chuma mdziko la South Africa, ati akuyembekeza kuti ndalama ya mlingo pa katundu ikhala pa 3.6 percenti mu zaka zitatu zikubwerazi. Akatswiriwa, alankhula izi potsatira kutenga nawo gawo mu kafukufuku yemwe ...anakhazikitsidwa ndi bungwe la Bureau for Economic Research. Bungweli, lati akatswiriwa ayankha motere potsatira boma kukhazikitsa ndondomeko zofuna kunetsetsa kuti mlingowu usakwere kuposera pa 3.7 percenti.
#Unduna oona za maboma aang'ono ang'ono mdziko la South Africa, wati uli odzipereka pa kufuna kuthandizira maboma aang'ono ang'ono mchigawo cha Mpumalanga omwe akulephera kulipira ngongole zawo ku kampani yopanga mphamvu za magetsi mdzikoli ya ESKOM. Maboma monga a Emalahleni, Govan Mbeki, Lekwa, Mbombela ndi Thaba Chweu, ndi mwa maboma ena omwe ali ndi ngongole ku kampaniyi ya ndalama zokwana $3.63 billion.
#Dziko la Japan, lakhala loyamba kuyamba kugwiritsira ntchito mafuta omwe anasunga potsatira kukumana ndi bvuto la kusowekera kwa mafuta. Mabvutowa, adza potsatira nkhondo yomwe ikuchitika pakati pa maiko a Iran, USA ndi Israel. Malonda a mafuta omwe amadutsa pa mtsinje wa Strait of Hormuz, akhudzidwa potsatira dziko la Iran kuletsa maboti ena ochokera mmaiko ena kupitiliza kudutsa pa mtsinjewu, zomwe zapangitsa mtengo wa mafuta kukwera pa dziko lonse.
Thamo Kapisa
Channel Africa News
#ZOCHITIKA
NKHANI ZATHU ZA LERO PA CHINYANJA SERVICE
#Nduna yoona za ubale ndi maiko ena mdziko la Kenya, Musaila Mudavadi, yati dzikolo pamodzi ndi dziko la Russia, agwirizana kuti nzika zake zisiya kutenga nawo gawo pa nkhondo yomwe ikuchitika pakati pa maiko a Russia ndi ...kraine. Nkhondo pakati pa maiko awiriwa, inayambika zaka zinayi zapitazo, ndipo lipoti lomwe linaperekedwa mu nyumba ya malamulo mdziko la Kenya mwezi watha, linatsonyeza kuti asilikali ochokera mdziko la Kenya osaposera 1 000 akutenga nawo gawo pa nkhondoyi. Mudavadi, walankhula izi pa mkumano omwe unachitikira mu mzinda wa Moscow mu likulu la dziko la Russia, ndi nduna ya za ubale ndi maiko ena ya mdziko la Russia , Sergei Lavrov.
#Presidenti wa dziko la USA, Donald Trump, wati dziko lake lili pa zokambirana ndi maiko asanu ndi awiri pa nkhani yofuna kuthandizira kukhazikitsa chitetezezo ku mtsinje wa Strait of Hormuz. Mtsinjewu, omwe uli mu mphepete mwa nyanja za Persian Gulf ndi Gulf of Oman ku maiko a ku aluya, wakhudzidwa ndi nkhondo yomwe ikuchitika pakati pa maiko a Iran, USA ndi Israel. Ma boti onyamula mafuta komanso katundu wina yemwe amadutsa mu mtsinjewu, asokonezedwa mayendedwe awo.
Nduna yoona za ubale ndi maiko ena mdziko la Germany, Johann Wadephul, walankhula kunena kuti bungwe la NATO lilibe cholinga chotenga nawo gawo pa nkhondoyi, koma zokambirana za chitetezo zomwe dziko la USA likufuna kuchita, zitha kukambidwa ndi maiko ena.
#Nzika za mdziko la Congo Brazzaville, zikudikra zotsatira za masankho oankha mtsogoleri zomwe zinachitika dzulo. Pa masankhowa, presidenti wa dzikolo Denis Sassou Nguesso, yemwe ali ndi zaka 82 zakubadwa, akuyembekezeka kupambana malingana ndi akatswiri pa nkhani za ndale. Mabungwe omwe anatenga nawo gawo pa kufuna kuonesetsa kuti masankhowa ayendetsedwa motsata ndondomeko, abwera poyera ndi kunena kuti chiwerengero cha anthu omwe anatenga nawo gawo chinali chochepa.
#Mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma ku Uganda, Robert Kyagulanyi, yemwe amadziwika kwambiri ndi dzina lakuti Bobi Wine, wanena kuti watuluka kwakanthawi m'dziko la Uganda atakhala pafupifupi miyezi iwiri akubisala.
Mu uthenga womwe anatulutsa Loweruka, iye anati anayamba kubisala pambuyo pa chisankho cha purezidenti cha mwezi wa Januwale chomwe akuti chinachitidwa mwachinyengo.
Iye wanenanso kuti magulu a chitetezo akumufunafuna komanso ankafufuza nyumba za anzake a ndale pomwe nyumba yake inali itazunguliridwa ndi chitetezo. Bobi Wine adati anatha kuthawa akuluakulu a chitetezo mothandizidwa ndi othandizira ake, ndipo watuluka kwakanthawi kuti akakumane ndi anzake a pa mayiko ena asanabwerere ku Uganda.
#Gulu la anthu omwe akuzitchula kuti ogwira ntchito m'boma ndipo ndi okhudzidwa mdziko la Malawi, lapereka masiku asanu kuti Public Service Pension Trust Fund (PSPTF) ibwezeretse K90 billion yomwe yagwira ntchito kugulira hotela ya Amaryllis.
Malingana ndi kalata yomwe yatulutsidwa lero yopita ku bodi ya PSPTF, gululi lati ma trustee a PSPTF alephera kuteteza zofuna za anthu ogwira ntchito m'boma ndipo ati bodi ikuyenera kuthetsedwa pompano, komaso maofesi awo atsekedwe kuti kafukufuku achitike mosavuta.
Mwazina, anthuwa akudandaula kuti sanadziwitsidwe za dongosolo lofuna kugula hotela ya Amaryllis.
Kuphatikiza apo, gululi likupempha kuti mamembala onse a bungweli ndi anthu omwe akuganiziridwa kuti apindula ndi mgwirizanowu amangwidwe, ponena kuti ayenera kuyankha milandu ali m'ndende kuti asakwanitse kubisa umboni.
Pamene ku nyumba ya malamulo, zokambirana za masanawa zinayamba ndi mtsogoleri wazipani zotsutsa boma munyumbayi a Simplex Chithyola Banda kupempha mtsogoleri wadzikolo a Peter Mutharika kuti achotse ntchito anthu ena omwe akutchulidwa mu nkhani za kugulitsidwa Kwa hotela ya Amaryllis.
Thamo Kapisa
Channel Africa News
#Zochitika
Nkhani za masewera
>Kazembe wadziko la South Africa mdziko la Algeria, watsimikiza kuti wadziwa za kumangidwa kwa Rulani Mokwena, nzika yadziko la South Africa, yemwe anali mphunzitsi watimu ya MC Alger yamdziko la Algeria, amene akuti anaphwanya malamulo adziko la ...Algeria okhudza ndalama. Akuti Mokwena anayimitsidwa ndi akuluakulu a kasitomu pa bwalo landege la Houari Boumediene mu mzinda wa Algiers, ponena kuti amafuna kutuluka mdzikolo ndi ndalama zakunja zomwe sanalembetse. Mokwena, omwe ndi wazaka makumi atatu, zisanu ndi zinayi, amachoka mdzikomo kuti akalumikizane ndi mzake wakale amene anasewera naye limodzi, komanso amene alinso nzika yadziko la South Africa, Thembinkosi Lorch, yemwe akusewera ndi timu yayikulu yamdziko la Libyah ya Al-Ittihad SC, atagawana zida ndi timu ya MC Alger patangotha myezi isanu ndi itatu yokha.
>Mphunzitsi wamkulu watimu ya Mamelodi Sundowns yamdziko la South Africa, Miguel Cardoso, wati timu yake ikadalira luso la osewera pamene akupita kukakumana ndi timu ya Stade Malien yamdziko la Mali, kumasewera awo akabwereza ampikisano wa CAF Champions League. Ngakhale Sundowns ili ndi mwayi wadzigoli zitatu itagonjetsa Stade Malien ndi dzigoli zitatu kwa ziro usiku walachisanu, mu mzinda wa Tshwane mdziko la South Africa, Cardoso akuyembekezera masewera ovuta kwambiri, makamaka masewerawo kuseweredwa pa bwalo la udzu opangidwa, kapena kuti artificial surface mchingerezi. Iye akukhulupilira kuti kuupeza, komanso luso, ndizofunika kwambiri kuti athe kukathana ndi vutoli. Popewa chipwirikiti, komanso pofuna kuti mayendedwe awo adzakhale osasokonekera, timu ya Sundowns idzagwiritsa ntchito ndege yawoyawo kupita ku Mali pamasewera akabwereza a lamlungu likibwerari.......
>Kafukufuku oyambilira amene watulutsidwa ndi mabungwe odziyimira pawokha wawonetsa kuti chiwerengero cha anthu omwe awonera mpikisano wa TotalEnergies CAF Africa Cup of Nations (AFCON) mdziko la Morocco wachaka cha 2025, chawonjezereka ndi 61 peresenti, kupangitsa mpikisano wa AFCON kukhala umodzi mwa masewera omwe akukula kwambiri padziko lonse. Lipoto lonse la mpikisano wa TotalEnergies CAF AFCON Morocco 2025 lidzatulutsidwa m'masabata akubwerawo ndi bungwe lakafukufuku lodziyimira palokha lapadziko lonse la Nielsen.
>Katswiri wamasewera a tennis amene ali pamwamba ku amayi, Aryna Sabalenka wamdziko la Belarus, ndi Jannik Sinner wamdziko la Italy yemwe ali pachiwiri ku amuna padziko lonse, anyamula zikho zawo zoyamba za mpikisano wa tennis wa Indian Wells Open mu mzinda wa California mdziko la United States of America. Sinner wagonjetsa Daniil Medvedev wamdziko la Russia mu ma fainali a amuna, pamene Sabalenka wagonjetsa Elena Rybakina wamdziko la Kazakhistani. Sinner wakhala mwamuna wachichepere oyamba kupambana mndandanda wamphotho zamipikisano ikuluikulu, kuphatikizirapo wa Australia Open ndi wa US Open, pamene Sabalenka wanyamula chikhochi atagonja mu ndime yomaliza kawiri konse kumbuyoku. Awiriwa tsopano maso ali ku mpikisano wa Miami Open omwe ukuyamba lachinayi.
Alex Nkhuku
Channel Africa News.
É hora de se atualizar com as últimas notícias e acontecimentos da atualidade no #Caleidoscopio com Mariamo Hassamo.
#ChannelAfrica
É hora de se atualizar com as últimas notícias e acontecimentos da atualidade no #Caleidoscopio com Mariamo Hassamo.
#ChannelAfrica
É hora de se atualizar com as últimas notícias e acontecimentos da atualidade no #Caleidoscopio com Mariamo Hassamo.
#ChannelAfrica
Join Mariamo Hassamo on #Caleidoscopio – a News and Current Affairs show that provides the latest updates on major news stories.
The show covers breaking stories as we round up all the news events of the day, especially on the African Continent between 20:00 – 21:00 CAT
...#ChannelAfrica
Subscribe to our newsletter and stay informed with the latest news, program highlights, and exclusive content from Channel Africa — a trusted voice in global broadcasting.
Channel Africa promotes Africa’s national interests through innovative content aiding the continent’s development. We deliver news, current affairs, and cultural programming globally, broadcasting in multiple languages to connect Africa to the world and the world to Africa.